Bungwe la Circle for Integrated Community Development-CICOD, lalimbikitsa ntchito yothana ndi njala mchigwa cha mtsinje wa Shire.

Takondwa Mangeni   15th Nov,2023

Story taken on Chivomerezi FM Facebook page

Bungwe la Circle for Integrated Community Development-CICOD, lalimbikitsa ntchito yothana ndi njala mchigwa cha mtsinje wa Shire.

Mwa zina, pa ntchitoyi, bungweli laika padera ndalama zokwana 12 million kwacha kuti zithandizire pa ulimi wa mchewere ndi mapira mmadela a mafumu akulu Ngabu komanso Masache mboma lino la Chikwawa.

Malingana ndi Edward Thole, yemwe ndi mkulu wa bungwe la CICOD, alimi pafufupi 2,500 ochokera mmaderawa, ndi omwe apindule ku thandizo la mbewu-zi, zomwe ndi za makono komanso zocha msanga.

Thole wauza wailesi ya Chibvomelezi kuti mlimi wina aliyense akulandira mbewu zolemera 1kg ya mapira komanso nchewere, mu ndondomekoyi yomwe yakhazikitsidwa kwa Mphenza mfumu yaikulu Ngabu mboma lino la Chikwawa.

Ndipo mmawu ake, Senior Group Village Headman Mphenza yalangiza anthu ake kuti asagulitse mbewu alandirayo, koma kuti ayidzale kuti adzasimbe lokoma patsogolo.

Pakali pano, Zione Mgoma, yemwe ndi mmodzi mwa alimi amene apindula nawo ndi thandizo la mbewu-li, wathokoza bungwe la CICOD kamba ka thandizoli.